Job 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono abwenzi ake a Yobe, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki, ndi Zofari wa ku Naama, adazimva za masoka onseŵa amene adamgwera. Ndiye tsiku lina anthu atatuwo adabwera, aliyense kuchokera kwao. Onsewo anali atapangana za nthaŵi yoti adzampepese ndi kudzamsangulutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abwenzi atatu a Yobu, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama, atamva za tsoka lonse limene linamugwera iye, ananyamuka ku nyumba zawo nakumana malo amodzi mopangana kuti apite ndi kukamupepesa Yobu ndi kumutonthoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za coipa ici conse cidamgwera, anadza, yense kucokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.