Job 20:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzabweza zimene adapata pogwira ntchito. Sadzadyerera chuma chake. Sadzapeza mpata wokondwerera phindu la malonda ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chimene adagwiriracho ntchito, adzachibweza, osachimeza; sadzakondwera monga mwa zolemera zake adaziona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cimene adagwiriraco nchito, adzacibweza, osacimeza; Sadzakondwera monga mwa zolemera zace adaziona.