Job 24:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale mai wake adzamuiŵala, koma mphutsi zidzasangalala pomudya. Momwemonso woipayo adzathyoka ngati mtengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera. Sadzamkumbukiranso; ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayi wowabereka amawayiwala, mphutsi zimasangalala powadya; anthu oyipa sakumbukiridwanso koma amathyoka ngati mtengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera. Sadzamkumbukilanso; Ndipo cosalungama cidzatyoledwa ngati mtengo.