Job 26:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akudzindikiritsa ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake; tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona! Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, awa ndi malekezero a njira zace; Ndi cimene tikumva za Iye ndi cinong'onezo cacing'ono; Koma kugunda kwa mphamvu yace akuzindikiritsa ndani?