Job 28:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amakumba njira zapansi mumgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu, mpaka kuiŵalika ndi anthu onka nayenda, amakhala ali lende pansipo, namazunguzika uku ndi uku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu; aiwalika ndi phazi lopitapo; apachikika kutali ndi anthu, nalendewalendewa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu, kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko; iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu; Aiwalika ndi phazi lopitapo; Apacikika kutali ndi anthu, nalendewa-lendewa.