Job 31:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindidaope zokambakamba za anthu kapena zonyoza za banja lina lililonse, sindidakhale chete kapena kubindikira m'nyumba chifukwa choopa iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza ndinaopa unyinji waukulu, ndi chipepulo cha mafuko chinandiopsetsa; potero ndinakhala chete osatuluka pakhomo panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa choopa gulu la anthu, ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ndinaopa unyinji waukuru, Ndi cipepulo ca mapfuko cinandiopsetsa; Potero ndinakhala cete osaturuka pakhomo panga.