Job 31:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ha, pakadakhala wina wondimva! Ndikulumbira kuti ndikulankhula zoona. Mphambe andiyankhe. Mdani wanga akadachita kulemba pa kalata mau ake ondineneza,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha! Ndikadakhala naye wina wakundimvera, chizindikiro changa sichi, Wamphamvuyonse andiyankhe; mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wanga!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aa, pakanakhala wina wondimva! Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe; mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha! ndikadakhala naye wina wakundimvera, Cizindikilo canga sici, Wamphamvuyonse andiyankhe; Mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wangal