Job 32:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakumvetseranidi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adatsutsa mau a Yobe, panalibe amene adayankhako nkomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde ndinasamalira inu; koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu, kapena wakumbwezera mau pakati pa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ineyo ndinakumvetseranidi. Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu; palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde ndinasamalira inu; Koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu, Kapena wakumbwezera mau pakati painu.