Job 32:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Elihu, mwana wa Barakele, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, adapsera mtima Yobe chifukwa chodziyesa wolungama kupambana Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi, wa chibale cha Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi, wa cibale ca Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.