Job 32:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Elihu, mwana wa Barakele wa fuko la Buzi, adayamba kulankhula, adati, “Ine ndine wamng'ono, inuyo ndinu akuluakulu. Nkuwona ndinkaopa, ndipo ndinkachita mantha kuti ndikuuzeni zakukhosi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi anayankha, nati, Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba; chifukwa chake ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati: “Ine ndine wamngʼono, inuyo ndinu akuluakulu, nʼchifukwa chake ndimaopa, ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi anayankha, nati, Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba; Cifukwa cace ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.