Job 34:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi Mulungu akuweruzeni potsata m'mene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Inu ndinu amene muyenera kusankha osati ine. Nchifukwa chake munene zimene mukudziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi chilango cha Mulungu chikhale monga muchifuna inu, pakuti muchikana? Musankhe ndi inu, ine ai; m'mwemo monga mudziwa, nenani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Chisankho nʼchanu, osati changa; tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi cilango ca Mulungu cikhale monga mucifuna inu, pakuti mucikana? Musankhe ndi inu, ine ai; M'mwemo monga mudziwa, nenani.