Job 34:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunali bwino aYobe akadayesedwa mpaka ku mapeto, chifukwa choti amayankha monga m'mene amayankhira anthu oipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha, chifukwa cha kuyankha kwake monga anthu amphulupulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha, Cifukwa ca kuyankha kwace monga anthu amphulupulu,