Job 4:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinthucho chidangoti chilili, koma ine osaŵazindikira maonekedwe ake. Patsogolo panga panali chinthu ndithu, kudangoti zii, kenaka ndidamva mau akuti:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unaima chilili, koma sindinatha kuzindikira maonekedwe ake; panali mzukwa pamaso panga; kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chinthucho chinayimirira koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani. Chinthu chinayima patsogolo panga, kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unaima ciriri, koma sindinatha kuzindikira maonekedwe ace; Panali mzukwa pamaso panga; Kunali cete, ndipo ndidamva mau akuti,