Job 4:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanji munthu amene adachokera ku dothi, amene ali fumbi chabe, amene amathudzuka ngati kadziwotche.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi, amene kuzika kwao kuli m'fumbi, angothudzulidwa ngati njenjete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi, amene maziko awo ndi fumbi, amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi, Amene kuzika kwao kuti m'pfumbi, Angothudzulidwa ngati gulugufe,