Job 42:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono abale ake onse ndi alongo ake omwe, kuphatikizapo onse amene ankamdziŵa kale, adabwera kwa iye nkudzadya naye chakudya m'nyumba mwake. Choncho adampepesa, namuthuzitsa mtima chifukwa cha mavuto onse amene Chauta adaalola kuti amgwere. Tsono aliyense mwa iwowo adampatsa ndalama ndi mphete yagolide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anamdzera abale ake onse, ndi alongo ake onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m'nyumba yake, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndalama ndi mphete yagolide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anamdzera abale ace onse, ndi alongo ace onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m'nyumba yace, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndarama ndi mphete yagolidi.