Job 42:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munandifunsa bwino kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mau opanda nzeru?’ Zoonadi ndidalankhula zimene sindidazidziŵe, zinthu zodabwitsa kwa ine zimene sindidazimvetse konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikira, zondidabwitsa, zosazidziwa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ukufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mawu opanda nzeru? Zoonadi ndinayankhula zimene sindinazimvetse, zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine zimene sindinazidziwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? Cifukwa cace ndinafotokozera zimene sindinazizindikira, Zondidabwiza, zosazidziwa ine,