Job 42:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta atalankhula ndi Yobe mau ameneŵa, adauza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira kwambiri pamodzi ndi abwenzi ako aŵiri, chifukwa simudalankhule zabwino za Ine, monga m'mene walankhulira mtumiki wanga Yobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova atayankhula ndi Yobu mawu amenewa anawuza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira pamodzi ndi abwenzi ako awiri, chifukwa simunayankhule zabwino za Ine, monga mmene wayankhulira mtumiki wanga Yobu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenera coyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.