Job 42:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsopano mutenge ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, mupite nazo kwa mtumiki wanga Yobe, mukaperekere nsembe zopsereza. Tsono mtumiki wangayo adzakupemphererani, pakuti pemphero lakelo ndidzalilandira kuti ndisakuchiteni kanthu potsata kupusa kwanu. Inu simudalankhule zabwino za Ine, monga adalankhulira Yobe mtumiki wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki Yobu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero tsopano mutenge ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi kupita nazo kwa mtumiki wanga Yobu kuti mukapereke nsembe zopsereza. Mtumiki wanga Yobu adzakupemphererani, ndipo Ine ndidzalandira pemphero lake. Sindidzakuchitirani kanthu molingana ndi uchitsiru wanu. Inu simunayankhule zabwino za Ine, monga anayankhulira Yobu mtumiki wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzambvomereza iyeyu, kuti ndisacite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenera coyenera monga ananena mtumiki Yobu.