Job 6:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi bulu amalira akakhala ndi msipu? Nanga ng'ombe, kodi imalira ikakhala ndi chakudya?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu? Ilira kodi ng'ombe pa chakudya chake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu, nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu? Ilira kodi ng'ombe pa cakudya cace?