Job 7:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndikachimwa, ndimakuvutani bwanji, Inu Wopenyetsetsa anthu? Chifukwa chiyani mwandiika kuti ndikhale ngati choponyerapo chandamale chanu? Chifukwa chiyani ndikukhala ngati katundu wolemera kwa Inu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani, Inu wodikira anthu? Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu? Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu, Inu wopenyetsetsa anthu? Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu? Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati ndacimwa, ndingacitire Inu ciani, Inu wodikira anthu? Mwandiikiranji ndikhale candamali canu? Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?