Job 7:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga ndi kundichotsera zolakwa zanga? Nthaŵi yoti ndiloŵe m'manda ili pafupi. Inu mudzandifunafuna, koma simudzandiwonanso.” Bilidadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga ndi kundichotsera machimo anga? Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda; mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundicotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kupfumbi; Mudzandifunafuna, koma ine palibe.