Joel 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu ansembe, valani ziguduli mudzigunde pa chifuwa chifukwa cha chisoni. Lirani, inu otumikira ku guwa. Tiyeni, mufunde ziguduli usiku wonse, inu atumiki a Mulungu wanga. Pakuti chopereka cha chakudya ndi chakumwa sizidzaonekanso ku Nyumba ya Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani; lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe. Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse, inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga; pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzimangire ciguduli m'cuuno mwanu, nimulire ansembe inu; bwnani, otumikira ku guwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'ciguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.