Joel 1:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Patulani tsiku losala, lalikirani masonkhano oletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya, itanani msonkhano wopatulika. Sonkhanitsani akuluakulu ndi anthu onse okhala mʼdziko ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu ndipo alirire Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Patulani tsiku losala, lalikirani masonkhano oletsa, sonkhanitsani akulu akulu, ndi onse okhala m'dziko, ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimupfuulire kwa Yehova.