Joel 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aononga mpesa wanga, athyolathyola mitengo yanga ya mikuyu. Aisadza, aikungunula makungwa, naŵataya, nthambi zake nkumazisiya zili mbee.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wawononga mphesa zanga ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu. Wakungunula makungwa ake ndi kuwataya, kusiya nthambi zake zili mbee.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nuukungudza konse, nuutaya; nthambi zace zasanduka zotumbuluka.