Joel 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ng'ambani mitima yanu, si zobvala zanu ai; ndi kurembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wacisomo, ndi wodzala cifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wocuruka kukoma mtima, ndi woleka coipaco.