Joel 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina mwake adzasintha mtima ndi kuleka, ndipo adzatisiyira madalitso. Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya ndi chakumwa zopereka kwa Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kaya, Yona kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni, nʼkutisiyira madalitso, a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa kwa Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pace, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yathira ya Yehova Mulungu wanu.