Joel 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sonkhanitsani anthu pamodzi, muŵauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m'chipinda mwao, abwere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sonkhanitsani anthu pamodzi, muwawuze kuti adziyeretse; sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Mkwati atuluke mʼchipinda chake, mkwatibwi atuluke mokhala mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akulu akulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati aturuke m'cipinda mwace, ndi mkwatibwi m'mogona mwace.