Joel 2:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe, amene ali atumiki a Chauta, azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde. Azinena kuti, “Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena aŵanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asaŵaseke pomafunsana kuti, ‘Ha, ali kuti Mulungu waoyo?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova, alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova. Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka, kuti anthu a mitundu ina awalamulire. Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti, ‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka colowa canu acitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulunguwao?