Joel 2:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaŵayankha anthu ake kuti, “Ndikutumizirani tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo mudzakhuta ndithu. Sindidzalolanso kuti akunja akunyozeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzawayankha kuti, “Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta ndipo mudzakhuta ndithu; sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzo kwa anthu a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ace, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale citonzo mwa amitundu;