Joel 2:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachotsa adani akumpoto kuti akhale kutali ndi inu, ndipo ndidzaŵapirikitsira ku dziko louma ndi lachipululu. Akutsogolo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuvuma, akumbuyo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuzambwe. Tsono mitembo yao idzatulutsa chivundi ndi fungo lonunkha. Zoonadi Chauta adachita zazikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu, kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu, gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo. Ndipo mitembo yawo idzawola, fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ndidzakucotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira ku dziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwace ku nyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwace ku nyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwace kudzakwera, ndi pfungo lace loipa lidzakwera; pakuti inacita zazikuru.