Joel 2:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu anthu a ku Ziyoni, kondwani ndi kusangalala chifukwa cha zimene Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani. Wakukomerani mtima pokupatsani mvula mofulumira. Wakupatsani mvula yochuluka, kumayambiriro ndi kumathero, monga pa masiku amekedzana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani, kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu, pakuti wakupatsani mvula yoyambirira mwachilungamo chake. Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka, mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula yamyundo, monga mwa cilungamo cace; nakubvumbitsirani mvula, mvula yamyundo ndi yamasika mwezi woyamba.