Joel 2:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mudzadya zambiri ndi kukhuta, ndipo mudzatamanda dzina la Chauta, Mulungu wanu, amene wakuchitirani zodabwitsa. Choncho anthu anga sadzaŵanyozanso ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anachita nanu modabwitsa; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta, ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu, amene wakuchitirani zodabwitsa; ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anacita nanu modabwiza; ndi anthu anga sadzacita manyazi nthawi zonse.