Joel 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kutsogolo kwake moto ukupsereza, kumbuyo kwake malaŵi a moto akutentha zinthu. Iwo asanafike, dziko linali ngati munda wa Edeni, koma atachoka, lidasanduka chipululu! Palibe kanthu kotsalapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patsogolo pawo moto ukupsereza, kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu. Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni, kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu, kulibe kanthu kotsalapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga cipululu copanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.