Joel 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulumpha pamwamba pa mapiri ndi phokoso longa la magaleta. Akumveka ngati malaŵi a moto otentha ziputu, ngati gulu lamphamvu lankhondo litakonzekera kumenya nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atumphako ngati mkokomo wa magaleta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akulumpha pamwamba pa mapiri ndi phokoso ngati la magaleta, ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu, ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atumphako ngati mkokomo wa magareta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.