Joel 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nthaŵi imeneyo ikadzafika, mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndipo kuzitunda kudzayenderera mkaka. Mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi. Kasupe adzatumphuka ku Nyumba ya Chauta ndi kuthirira chigwa cha Sitimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsiku limenelo mapiri adzachucha vinyo watsopano, ndipo zitunda zidzayenderera mkaka; mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi. Kasupe adzatumphuka mʼnyumba ya Yehova ndipo adzathirira Chigwa cha Sitimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi a kasupe adzaturuka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi cigwa ca Sitimu.