Joel 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma Ejipito adzasanduka chipululu, ndipo Edomu adzakhala bwinja lopanda anthu, chifukwa cha nkhondo imene adathira pa anthu a ku Yuda ndiponso chifukwa cha kukhetsa magazi a anthu osalakwa ku dziko lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m'dziko lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Igupto adzasanduka bwinja, Edomu adzasanduka chipululu, chifukwa cha nkhondo imene anathira anthu a ku Yuda mʼdziko limene anakhetsa magazi a anthu osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aigupto adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka cipululu copanda kanthu, cifukwa ca ciwawaci anawacitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosacimwa m'dziko lao.