Joel 3:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yonse, ndipo ndidzaŵatengera ku chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzaŵaweruza chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, osankhidwa anga, pakuti adaŵamwaza m'maiko ao onse, nagaŵana dziko langa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzawaweruza chifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli, pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthu ndikugawa dziko langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao ku cigwa ca Yosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi colowa canga Israyeli, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa,