Joel 3:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi inu a ku Tiro, a ku Sidoni ndi a ku madera a Filistiya, mukuti mundichite chiyani? Kodi mumati mundilipsirire chifukwa cha zina zimene ine ndakuchitani? Ngati pali kanthu koti mundilipsirire, ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu mofulumira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Afilisti? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso ndiri ndi ciani ndi inu, Turo ndi Zidoni, ndi malire onse a Afilisti? mudzandibwezera cilango kodi? Mukandibwezera cilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera cilango canu pamutu panu,