Joel 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzaŵagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali aja. Ndatero Ine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzagulitsa ana ako amuna ndi akazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutari; pakuti Yehova wanena.