John 1:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yohaneyo adaamchitira umboni. Ankauza anthu mwamphamvu kuti, “Uyu ndiye uja ndinkanenayu kuti amene akubwera pambuyo panga ngwoposa ine; pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yohane achitira umboni za Iye. Iye akufuwula kuti, “Uyu ndi Iye amene ndinati, ‘Iye amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa, Iyeyo analipo ine ndisanabadwe.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yohane acita umboni za iye, napfuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; cifukwa anakhala woyamba wa ine.