John 1:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikhalire palibe munthu amene adaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekha uja, amene ali wapamtima wa Atate, ndiye adaulula za Mulunguyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.