John 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamufunsa kuti, “Nanga iwe ndiwe yani? Kodi ndiwe Eliya?” Iye anati, “Sindine.” “Kodi ndiwe Mneneri?” Iye anayankha kuti, “Ayi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye, Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.