John 10:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthaŵa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa si zake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa siziri zace za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;