John 10:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adamuyankha kuti, “Sitikufuna kukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ai, koma chifukwa ukunyoza Mulungu. Iwe, amene uli munthu chabe, ukudziyesa Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ayuda anamyankha iye, Cifukwa ca nchito yabwino sitikuponyani miyala, koma cifukwa ca mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu,