John 10:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mau a m'Malembo ngoona mpaka muyaya, ndipo Mwiniwakeyo adaŵatcha milungu anthu aja Iye ankalankhula nawoŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati anawacha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo colemba sicingathe kutyoka),