John 10:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inetu Atate adandipatula nandituma pansi pano. Tsono inuyo munganene bwanji kuti ndikunyoza Mulungu, chifukwa ndati ndine Mwana wa Mulungu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma ku dziko lapansi, Ucita mwano; cifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?