John 10:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati ndimazichitadi, khulupirirani ntchitozo, ngakhale simukhulupirira Ine. Apo mudzadziŵa mosapeneka konse kuti Atate amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa Atate.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati ndicita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani nchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi ine mwa Atate.