John 10:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ambiri adadza kwa Iye, nkumanena kuti, “Yohane sadachite chizindikiro chozizwitsa ai, koma zonse zimene ankanena za Munthuyu zinali zoonadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ambiri anadza kwa iye; nanena kuti, Sanacita cizindikilo Yohane; koma zinthu ziri zonse Yohane ananena za iye zinali zoona.