John 11:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene anali m'nyumba akupepesa Mariayo, ataona kuti wanyamuka msangamsanga ndi kutuluka, adamtsatira. Ankayesa kuti akupita kumanda kukalira kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Maria ananyamuka msanga, natuluka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.