John 11:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo akulu a ansembe ndi Afarisi adaitanitsa Bungwe Lalikulu la Ayuda, nafunsana kuti, “Titani pamenepa, popeza kuti munthuyu akuchita zozizwitsa zambiri?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anayitanitsa msonkhano wa akulu olamulira. Iwo anafunsa kuti, “Kodi ife tikuchita chiyani? Pano pali munthu uyu akuchita zizindikiro zodabwitsa zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ansembe akulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? cifukwa munthu uyu acita zizindikilo zambiri.